Psalms 15

Salimo la Davide.

1Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika?
Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera?

2Munthu wa makhalidwe abwino,
amene amachita zolungama,
woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,
3ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira,
amene sachitira choyipa mnansi wake
kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,
4amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa.
Koma amalemekeza amene amaopa Yehova,
amene amakwaniritsa zomwe walonjeza
ngakhale pamene zikumupweteka,
5amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja
ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa.

Iye amene amachita zinthu zimenezi
sadzagwedezeka konse.
Copyright information for NyaCCL